Zamaboma
©ZaMmaboma
Banja lina akulilozerana pa mudzi wina kwa Sub T/A Mkagula m’boma la Zomba. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli banja lina lomwe anthu ankalipatsa ulemu kwambiri. Koma masiku apitawo mwamuna wapa banjalo anapita kudimba ndi mlamu wake, yemwe ndi m’longo wake wa mkazi wake. Ndipo ali kudimba komweko mlamu wakeyo anagwa pansi, imfa nkukhala yomweyo. Uthenga wa zovutazo utafika kumudzi anthu onse anali odabwa kamba koti pomwe awiriwo amachoka pakhomopo m’nyamatayo sanadandaule kuti pena pamamutsina. Atafika pakhomo ndi zovutazo anthu anapitiriza ndi mwambo wamaliro posambitsa thupilo. Koma atasambitsa mtembowo chidebe chomwe amasambitsira mtembowo chinasowa pasiwapo mosadziwika bwino. Ngakhale mikoko yogona inayesetsa kuchifuna-funa chidebecho palibe munthu ndi m’modzi yense yemwe anavomera kuti ndiye watenga chidebecho. Apo mwambo wamaliro unayamba waima kwa kanthawi mpaka pomwe eni mbumba anaitana katakwe wina wa mankhwala a zitsamba yemwe atachira mtera wake anapeza kuti mmodzi mwa achibale a malemuwo ndiye wasowetsa chidebecho. Ndipo atafufuza anapeza chidebecho chiri kunsi kwa kama m’chipinda chogona cha mlongo wake wotisiyayo yemwe mwamuna wake anali ndi womwalirayo kudimba. Apo mpungwe-pungwe unabuka pasiwapo. Zinatengera mikoko yogona kukhazikitsa bata ndipo mwambo wamaliro unapitilira. Pakadali pano mikoko yogona mderalo yati itengera banjalo kubwalo mwambo wa zovuata ukangotha. Koma anthu onase pa mudzipo akuloza zala banjalo kuti likudziwapo kanthu paza imfa ya m’nyamatayo.
No comments:
Post a Comment